Chichewa Christian Hymns
Hymn 321 PAKUONA imfayo
PAKUONA imfayo
Chisonicho chikula
Ndilira misozi.
Ndilira, ndilira,
Ndilira Mbuye Yesu wangadi.
Ndaimba ndi kulira ndi kusisima,
Ndaimba ndi kulira ndi kusisima,
Ha! Ha! Aleluya!
Ha! Ha! Aleluya!
Mwasiyiranji Ambuye Yesu?
Ndinasiya amayi,
Ndinasiya atate,
Abale komweko.
Kazembe wanga m’matenda,
Ndili m’manja mwa Mbuye.
Abale tsalani.
Zoipa zakanikadi,
Sizikhoza kuchotseka,
Ndilira misozi.
Angelo aitana,
Aitana Kumwambako,
Tiyeni, tikwere!
Munafera pa mtanda
Chifukwa cha inedi,
Si cha wina ayi.