Chichewa Christian Hymns
Hymn 10 TSOPANO linoli,
TSOPANO linoli,
Tiimbe nyimbo zathu;
Tiimbe nyimbozi,
Titame Mlungu wathu.
Masiku onsewo, Anatisungadi,
Anatipatsanso, Zabwino zonsezi.
Mulungu yemweyo
Akhale m’fupi mwathu;
Mtendere wakewo,
Ukhale m’mtima mwathu.
Tim’tsate Iyedi, Ndi nsoni zakezo;
Panjira yakeyi, Masiku onsewo.
Tilemekezetu, Atate wa Kumwamba;
Ndi Yesu Mbuyathu, Ndi Mzimu Wakuyera;
Mulungu Mmodziyu, Wanthaŵi zonsezo;
Tim’lemekezetu, Masiku onsewo.