Chichewa Christian Hymns
Hymn 92 KONDA dzinalo la Yesu,
KONDA dzinalo la Yesu,
Mwana wosawuka’we;
Ndilo lothandiza anthu,
Khala nalo ponse phee.
Dzina la Yesuyo,
N’lokondwetsa onsewo;
M’mwambamo, ponsepo,
Litonthoza m’mtimamo.
Konda dzinalo la Yesu,
M’moyo mwako monsemo;
Mmene ulikuyesedwa,
Tchula dzina lakelo.
Dzina ili ndi lokoma,
La Mtetezi wathuyo;
Mmene adzatilandira,
M’mwamba tidzakondwadi.
Mbuye Yesu tim’tamanda,
Ndi nyimbo zathu zonse;
Mfumu ya mafumu onse,
Yesu timayesadi.