Chichewa Christian Hymns
Hymn 66 >ALELUYA, Aleluya, Aleluya!
ALELUYA, Aleluya, Aleluya!
Nkhondoyo yatha, imfa yagonja,
Yesu wamoyo anaiposa,
Msampha woipa wonse nawonja,
Aleluya!
Mphamvu za imfa ndi za Satana
Naye Ambuye zinalimbana,
Komatu Yesu anapambana.
Aleluya!
Atha masiku aja ansoni,
Mbuye wauka, ali ndi mboni;
Lero chimwemwe, chatha chisoni,
Aleluya!
Nsinga za imfa Iye ’nadula,
Khomo la m’Mwamba, nalitsegula;
Yesu timtama tonse tipfuula,
Aleluya!
Mbuye mabala anu olimba
Atichotsera mantha a imfa;
Tsono ndi mtima wonse tiiimba:
Aleluya!