Chichewa Christian Hymns
Hymn 52 POTULUKA m’mudzimo
POTULUKA m’mudzimo
Yesu anasenza mtanda,
Pokwera ku Gologota
Kukampachikatu Mbuye.
Pilatoyo, mfumu yawo,
Inampereka kwa ’Yuda,
Kuti ampachiketu
Kufera zoipa zathu.
(Atate ’nu amayi ’nu, nonsenu,
Onani Yesu wasenza mtanda;
Atate ’nu, amayi ’nu, nonsenu,
Onani Yesu wasenza mtanda.)
Zoopsya zopambana
Zinachtika pamtanda
Kuti mdima unadza,
Dzuŵa linabisikanso.
Chinsalucho cha m’kachisi
Chinang’ambika pakati,
Myala inaswekanso,
Dziko linagwedezeka.
Pomwalira Mbuyeyo
Anapfuula kokweza
Naitana atate
Kupereka mzimu wake:
“Mlungu wanga, Mlungu wanga.
Mwandisiy’ranjitu Ine,
Mundikweze m’Mwambamo,
Landirani mzimu wanga.”
Ankhondowo poona
Zinachitika pamtanda,
Anabaya m’nthitimo,
Munatuluka magazi.
Paphirilo la Golgota
Anaferapo Mbuyeyo
Nasauka koopsya
Ndi zoipa zathu izi.