Chichewa Christian Hymns
Hymn 458 USIKUWO, woyerawo!
USIKUWO, woyerawo!
Mwana adam’lerayo;
Akakhale Mfumuyo,
Anabadwa m’kholamo,
Mfumu ya mafumu,
Ndi ya anthuwo.
Mwanayo wa Mlunguyo,
Andikonda inetu;
Nan’tayira chumacho,
Nadzagona mu’dzumo,
Ndiyamika Mbuye,
Wanga Yesuyo.
Usikuwo, woyerawo!
Wadzatu mtenderewo;
Ife tonse anthuwo,
Atitenga Mlunguyo,
M’lemekeze “Tate,
Mwana, Mzimunso.