Chichewa Christian Hymns
Hymn 428 MBUYE mtsitsimutse
MBUYE mtsitsimutse
Ntchito zonse zanu!
Utsani anthu akufa
Ndi mawu a mphamvu.
Mbuye mtsitsimutse
Ntchito zonse zanu!
Tauzirani pa ife
Ndi mweya wa Mzimu
Mbuye mtsitsimutse
Ntchito m’mitimamo!
Mumvetse njala kwa Inu—
Mutikhutitsenso.
Mbuye mtsitsimutse
Ntchito m’kati mwa anthu!
Chikondi chawo chikule
Muchikolezetu.
Mbuye mtsitsimutse!
Mawu alimbike,
Pamene aphunzitsidwa
Onsewa amvere!
Mbuye mtsitsimutse!
Mzimu adzazetu!
Kwa ife kudzakhala mwayi,
Kwa Inu ulemu.