Chichewa Christian Hymns
Hymn 401 A MULUNGU,
A MULUNGU,
Munatuma Yesuyo,
Mwana wanu Yekhayo.
Anabadwa,
Anabadwa motere,
Monga mmphaŵi m’kholamo.
Anakonda
Anakonda anthuwo,
Naŵapulumutsanso.
Anafera,
Anafera m’mtandamo,
Anafera ifenso.
Anadzuka
Anadzuka m’mandamo,
Anatenga moyowo.
Anakwera,
Anakwera m’Mwambamo
Kwa Mulungu ’Tatewo.
Adzabwera,
Adzabwera Iyeyo
Tsiku lomalizalo.
Aleluya,
Aleluya Yesuyo,
Tizitama dzinalo.