Chichewa Christian Hymns
Hymn 370 KWACHA lero kwati mbee,
KWACHA lero kwati mbee,
Tsiku la Mulunguli;
Dzuŵa liŵaliradi
Thambo ndi zapansipa
Upumira mpweyawu
Wa Mulungu konseku.
M’nyumba yanu, Mlungu, ’yi
Tisonkhana teretu,
Ndi mitundu yonseyi
Tikulambireni ’Nu:
Yesu Mbuye wathuyo
Ndiye Mfumu ponsepo.
Inu Mlungu kalelo
Mutalenga zonsezi
Munapuma tsikulo;
Tipumadi ifenso.
Mommo tilandiratu
Zopumitsa mtimawu.
Yesu munadzukanso
M’manda lero lomwetu;
Ntchito munayambayo
Yakudzutsa anthu ’fe,
Kuti ndi mitimayi
Tigwirebe ntchitozi.