Chichewa Christian Hymns
Hymn 359 TADZUKA mzimu wanga ‘we,
TADZUKA mzimu wanga ‘we,
Ugwire ntchito zakozi;
Kukondwa ukutengedi,
Pemphero ulikwezedi.
Pemphero, pemphero,
Pemphero ulikwezedi;
Pemphero, pemphero,
Pemphero ulikwezedi.
E, nthawi ya m’mamaŵayi,
Um’tamandire Mbuyeyo;
Nuyese lero ngatitu,
Tsiku lakumalizalo.
Munkhani zako zonsetu,
Unene molungamadi;
Nudziwe kuti Mbuyako,
Adziwa zachinsinsizi.
Patsikuli, Mbuyanga ‘Nu.
Munditsogoze m’njiramo;
Ulemelero wanuwo,
Undilimbitse monsetu.
Tim’lemekeze Mlunguyu,
Wamadalitso onsewo;
Tim’lemekeze tonsefe,
Atate, Mwana, Mzimunso.