Chichewa Christian Hymns
Hymn 346 PEMPHERO ndiko kufuna,
PEMPHERO ndiko kufuna,
Kulakalakatu;
Ndi monga moto liyaka
Mumtima wa munthu.
Pemphero ndiko kulira,
Ngakhale misozi,
Kupenyetsetsa Kumwamba,
Mulungu mpafupi.
Pemphero ndiko kufuna
Kwa mwana wamng’ono;
Ndiponso mawu amphamvu
A munthu wamvanu.
Pemphero ndiwo mweyawo
Apuma akristu;
Ndi mapemphero tiloŵa
Dziko la imfalo.
Mutiphunzitse, Mbuyathu,
Kupempha kotero,
Kuyandikira kwa Mlungu
Ndi mtima wabwino.