Chichewa Christian Hymns
Hymn 335 KWATHU sipadziko, ndingopitilira,
KWATHU sipadziko, ndingopitilira,
Ndadzikundikira chuma Kumwambako;
Mngelo akodola pakhomo la M’mwamba,
Ndipo dziko lapansi sindiyesa kwathu.
Mbuye, ndi ‘Nu Bwenzi langa ndithu.
Ndichitenji ngati Kumwamba sikwathu?
Mngelo akodola pakhomo la M’mwamba,
Ndipo dziko lapansi sindiyesa kwathu.
Andiyembekeza, chinthuchi ndidziwa,
Mpulumutsi wanga wandikhu’lukira;
Adzandipyoletsa pamene ndafoka,
Ndipo dziko lapansi sindiyesa kwathu.
Mbuye watsogola ku Ulemerero,
Ndifuna kugwira dzanja lake konko;
Andidikiranso pakhomo la M’mwamba,
Ndipo dziko lapansi sindiyesa kwathu.
Mu Ulemelero tidzakhala m’yaya,
Oyera mtimawo ali kulambira;
Ati: “Aleluya kwa Mlungu wamphamvu,”
Ndipo dziko lapansi sindiyesa kwathu