Chichewa Christian Hymns
Hymn 333 M’DZIKO lino tikhalamo
M’DZIKO lino tikhalamo
Utibvuta moyo,
Koma dziko la mtendere
Lili kwa Mulungu.
Watitsogolera Mbuye,
Komwe kwa Atate,
Ndimo tidzatsata naye
Moyo wathu wonse.
Ndi tsopano tilindira
M`dziko lathu lino;
Ntchito atipatsa Mlungu,
Tizigwira bwino.
Ngati zakuipa zathu
Zikatisautsa,
Tithaŵire kwa Mbuyathu,
Atipulumutsa.
Timpemphere kutipatsa
Mtima watsopano,
Kutithandizira kunka
Paulendo uno.