Chichewa Christian Hymns
Hymn 318 TINALI ambiri ife,
TINALI ambiri ife,
Enatu anatisiya;
Chisoni mumtima mwanga.
Amayi, abambo, apita,
Anyamata, atsikana, apita;
Chisoni mumtima mwanga.
Bwera mbale wangawe,
Msangatu kwa Mbuye wako;
Chisoni mumtima mwanga.
Zoipa za m’dziko lino,
Zikusokeretsa anthu;
Chisoni mumtima mwanga.
Bweratu mbale wangawe,
Utsate Ambuye Yesu;
Upeze moyo wosatha.