Chichewa Christian Hymns
Hymn 317 UKATHA moyo wanga
UKATHA moyo wanga
Kumwamba kundichera;
Dzuŵalo ndimalira
Lafika lokomera.
Usiku m’nali mdima,
Tsopano mbanda kucha;
Kudzaŵalitsa ndithu
Ku Dziko la Mulungu.
Chitsime chachikondi
Ndi Yesu Mbuye wanga;
Ndalaŵa mtsinje pano
Ndzamwetsa ine m’Mwamba.
Komweko zidzakula
Chisomo ndi chifundo,
Pondiŵalira kuja
Ku Dziko la Mulungu.
A! Yesu Bwenzi langa
Inenso bwenzi lake,
Woipa ’ne alola
Ndiloŵe m’nyumba mwake;
Ndikhulupira Iye
Achotsa mphulupulu;
Kudzandiŵalitsira
Ku Dziko la Mulungu.
Ambuye andisunga
M’chifundo chachikulu;
Zisoni zisanduka
Chimwemwe cha Mulungu.
Dzanjalo ndilitama
Ndi mtima wachifundo,
Mpakatu kwaŵalitsa
Ku Dziko la Mulungu.