Chichewa Christian Hymns
Hymn 316 NDAMVATU kuti tifika komweko
NDAMVATU kuti tifika komweko
Kuli Ambuye, Mtetezi wathuyo.
Ine, pakutha zobvuta zathuzo
Iye tidzamwona maso ndi maso.
Ndi Mbuyeyo tikhalamo,
Kupenyanso wokondatu;
Tidzakondwera, E, nthaŵi zonsezo
Ndicho chimwemwe ndi ulemutu.
Kaamba chisomo cha Mbuyathu uyu,
Malo okoma tipeza m’Mwambamo;
Kumva mtetezi amene ndi Yesu,
Ndicho chimwemwe ndi chachikulutu.
Onse aliko takonda kalelo,
Kale napita kwa Yesu Mbuyawo;
Koma kumwona Mtetezi wathuyo
Ndicho chimwemwe choposa, nchathucho.