Chichewa Christian Hymns
Hymn 301 MBUYE, ndapangana
MBUYE, ndapangana
M’njira yanuyi,
Kuti ndidzayenda
Osaleka ’yi.
Mundipatse mtima
Wopiriramo,
Wakukana zonse
Zondipingazo.
Mzimu wakuipa
Undiyesa ’ne;
Mundithangatire
Ku’thaŵitsabe.
Akandisautsa
Kum’dzi kunoku,
Muloŵetse mphamvu
M’mtima mwangamu.
Akathira nsembe Ku mizimuyo,
Ndipenyera kwanu,
E, Kumwambako.
Tsoka ndi zonyenga
Za ufitizo,
Yesu mndilimbitse
Ndisaopezo.
Pena kumwa nawo,
Ndisateroko,
Pena kukaona
Gule woipa,
Pena kuwombeza
Sindifuna ’yi;
Yesu mundithandize
Kuzikanazi.
Ndinu mbusa wanga;
Mndithandizetu;
Ndisaipse nazo
Mtima wangawu.
Osaopa konse,
Osachimwa ’yi.
Mundiyendetse Yesu
M’njira yanuyi.