Chichewa Christian Hymns
Hymn 296 TIYENI Akhristu,
TIYENI Akhristu,
Nkhondo tigwire;
Yesu Mbuye wathu
Atitsogolera.
Mfumu yathu mwini
Atipatsa moyo;
Taonanitu mbendera
Yailoŵa nkhondo!
Tiyeni Akristu,
Nkhondo tiigwire;
Yesu Mbuye wathu
Atitsogolera
Nkhondo ya Satana
Idzakuthaŵani;
Tiyeni Akristu,
Kaipambaneni.
Idzanjenjemera
Mukapfu’litsatu;
Imbitsanitu anzathu,
Mau mukwezetse.
Mpingo wa Mulungu
Uli ngati nkhondo;
Titsagane nawo
Ana a Mulungu.
Sitipatukana,
Ndifetu amodzi;
Ch’yembekezo, chikondano,
Chonse ndi chimodzi.
Zonse zapadziko
Zidzamalizira,
Koma mpingo wake
Uli chikhalire;
Udzakhala ndithu
Mphamvu za Satana,
Yesu analonjezetsa,
Mawuwo sakana.
Tiyeni anzathu
Tizithandizana;
Imbirani nafe
Nyimbo zopambana
Kristu ayenera
Mphamvu ndi ulemu;
Komwe kuli Yesu.