Chichewa Christian Hymns
Hymn 292 NDIPULUMUTSENI Mbuye,
NDIPULUMUTSENI Mbuye,
Madzi afikira moyo wanga.
Ine ndayimilira m’thope lozama,
Popanda popondera;
Ine ndalowa m’madzi ozama,
Ndipo chigumula chandipeza.
Ndalema ndi kufuula,
Ndipo kummeroku kwauma gwaa!
M’maso mwanga mwada bii,
Kuyembekezera Mlungu wanga.
Ndilanditsenitu,
Mbuye,
Kwa adani anga ondilonda.
Mundiyankhe Yehova’Nu,
Monga mwakukoma mtima kwanu.