Chichewa Christian Hymns
Hymn 290 NAMONDWE wawuka,
NAMONDWE wawuka,
Pakati panyanja;
Tiwoloke bwanji,
Kupita kutsidya;
Yesu ayitana,
Tikamvere Mawu.
(M) Akhrisitu mukupita kuti?
(O) Tikupita kutsidya,
Kutsidya la nyanja.
Yesu ayitana tikamvere Mawu.
Namondwe wauka,
Pakati panyanja;
Tiwoloke bwanji,
Kupita kutsidya;
Yesu analetsa,
Namondwe panyanja.
Namondwe wawuka,
Pakati panyanja;
Tiwoloke bwanji,
Kupita kutsidya;
Yesu alonjeza,
Kutiwolotsatu.