Chichewa Christian Hymns
Hymn 245 KHALANI duu! Ambuye adzatu;
KHALANI duu! Ambuye adzatu;
Senzani chete mtanda wanuwu;
Mulungu adzakonza zanuzo,
Sangasinthike mtima Iyeyu.
Khalani duu! Bwenzilo Yesuyo
Atsogolera m’njira mwathumu.
Khalani duu! Mulungu wanuyu
Akonzeratu nthaŵi zonsedi;
Musakayike mtima; zo’psyazo
Zimasulidwa pomalizapo.
Khalani duu! A Yesu Mawuwo
Ngamphamvu lero monga kalelo.
Khalani duu! pakufa mnzathuyo,
Pakumlirira ndi misoziyo;
Pa nthaŵizo abwera Yesutu,
Mitima yathu natonthozadi.
Khalani duu! Ambuye athadi
Kutibwezera zochotsedwazi.
Khaladi duu! pakufa ifetu,
Ndi Yesu tidzakhala indetu
Popanda mantha ndi zoŵaŵazi,
Chikondi chokha koma m’mtimamo.
Khalani duu! pakutha zonse phe
Tidzasonkhana tonse kuli ’Ye.