Chichewa Christian Hymns
Hymn 17 MULUNGU ndiye Mbusa wanga,
MULUNGU ndiye Mbusa wanga,
Sindisoŵa konse;
Amandiŵeta nandidyetsa,
Nandipatsa zonse.
(Ndiye Mbusa wanga,
Ndiye Mbusa wanga!
Mulungu ndiye Mbusa wanga,
Sindisoŵa konse)
M’mitsinje yamtendere mtima,
Wanga aumwetsa;
Mapazi omwe m’njira,
Yolungama nayendetsa.
Za mdima, imfa, nkhondo ndi zoipa sindiopa;
Ndikakhumudwa ndi kutopa,
Andipulumutsa.
Podwala ine, povutidwa,
Andisamalira;
Pondisautsa ’dani anga
Nandithangatira.
Chisomo ndi zokoma zake,
Sizileka konse;
Ndi m’nyumba ya Mulungu,
Ndidzakhala nsiku zonse.