Chichewa Christian Hymns
Hymn 157 INU nonse ovutidwa,
INU nonse ovutidwa,
Mbuye ali panopa;
M’maso mwanu muli msozi,
‘Dzani kwa Mbuyathuyo.
Yesu ngwachifundodi,
E! Wafera inutu;
E! Wafera inutu.
Yesu ndiye Bwenzi lanu,
Ali wachikondicho;
Kodi inu mum’kanabe?
M’lape msanga m’mtimamo.
Pena imfa idza mawa,
Manda ali mfupimo;
Nthawi ino ndi yabwino,
Mlole Yesu m’mtimamo.
Ndi angelo a Kumwamba,
Anke ndi uthengawo;
Kuti wina wadza lero,
Kwa Mbuyathu Yesuyo.