Chichewa Christian Hymns
Hymn 132 MVERA mtima wanga ’we
MVERA mtima wanga ’we
Akufunsa Ambuye;
“Wosauka wa’mphaŵi,
Kodi undikondadi?”
“Ndakupeza womanga,
Ndamasula zinsinga,
Ndakulonda kutali,
Kodi undikondadi?”
“Akaleka amake
Kusungira mwanake,
Ine sin’kuleka ’yi,
Kodi undikondadi?”
“Ndakukonda ku imfa
Ndi chikondi chosatha,
Kwaulere, kwambiri,
Kodi undikondadi?”
“Msanga ndidzabweratu,
Udzaona ulemu,
Udzakhala ndi Ine,
Kodi undikondadi?”
Mbuye ndisaukadi,
Chimachepa chikondi,
Mtima wanga mudziŵa,
M’ndipunzitse kukonda.