Chichewa Christian Hymns
Hymn 114 NDIPO Eliya anati kwa Elisa:
NDIPO Eliya anati kwa Elisa:
“Ukhale pano ndipita ku Beteli.”
Ndipo Elisa anati kwa Eliya:
“Sindidzakusiyani.”
Ndipo Eliya anati kwa Elisa:
“Upemphe chimene ndidzakuchitira.”
Ndipo Elisa anati kwa Eliya:
“M’ndipatse Mzimu wanu.”
Ndipo Eliya anali munthu mnzathu,
Nanga mbalewe uchedwera chiyani;
Sintha mtima ukhale ngati Elisa,
Udzapulumutsidwa.