Chichewa Christian Hymns
Hymn 103 MPUME pa inetu, Mpweya wa Mulungu,
MPUME pa inetu, Mpweya wa Mulungu,
Ndi kundidzaza moyo wanuwo,
Kuti ndikonde zomwe mukondanso,
Ndichite chomwe mumachitanso.
Mpume pa inetu, Mpweya wa Mulungu,
Mpaka mtimanga ukayeretu,
Ndipo zokhumba zanga zilingane
Nazo zanuzo zakuyera mbuu!
Mpume pa inetu, Mpweya wa Mulungu,
Mpaka ndikhale wanu nokhatu;
Ayeretsedwe makhalidwe anga
Ndi mphamvu yanu yondisunga nji!
Mpume pa inetu, Mpweya wa Mulungu,
Kuti inedi ndisafe ’yitu,
Koma ndikhale nanu m’moyo womwe
Wangwiro ndi wa nthaŵi zonsetu.