Chichewa Christian Hymns
Hymn 65 NLA Mlungu dzuŵali:
NLA Mlungu dzuŵali:
Pa mbanda kuchapo
Angelo ‘nadzatu
Nachotsa mwalawo.
Ndi mtima wonse mwimbedi,
‘Nauka Mbuye leroli.
Alonda onsewo
‘Nagwidwa manthadi
Poona zo’psyazo
Zoonekerazi.
Mulibe m’mandamu,
Wadzuka Mbuyetu;
Woposa imfayo
Ndi Mwini moyowu.
Dzukani nayetu,
Oyera inunso,
Lekani m’mandamo
Zakufa zanuzo.
Titama Yesuyo,
Ambuye m’Mwambamo,
Wofera anthu ’Ye,
Timkondakondako.