Chichewa Christian Hymns
Hymn 80 KUDZA kwa Mbuye
KUDZA kwa Mbuye
kudzatero monga mphenzi,
Ing’anima M’mwamba choncho Iye,
Dziko lidzanjenjemera oyipa onse,
Nayamba kuthawa powona Iye.
Yesu akhala pampando,
Kuweruza makamuwo;
Nkhosa dzanja lamanjalo,
Mbuzi kudzanja lamanzelero.
Ayimba kumpando’ko wolemekezeka,
Mfumu ya Kumwamba
Mbuye Yesu,
Alira m’Gehenamo moto, moto, moto,
Ndipeze kuti madzi akumwa.
Udzachitanji mbale pobwera Ambuye,
Kudzaweruza dziko lapansi,
Ngati sudakonzeke khulupira Yesu,
Kuti upeze moyo wosatha.