Chichewa Christian Hymns
Hymn 67 PAMENEPO pokhala madzulo,
PAMENEPO pokhala madzulo,
Tsiku loyamba la Sabata;
Chifukwa chakuopa a Yuda,
Makomo ali chitsekere.
Yesu anadza naimilira,
Pakati pa ophunzirawo,
Yesu nanena mawuwo nati:
“Mtendere ukhale ndi inu.
Pameneponso Yesu Ambuye,
Naonetsatu Tomasiyo;
Manja akewo ndi nthiti zake,
Tomasi nati: “Mlungu wanga.
Odala iwo okhulupira,
Ngakhale iwo sanaone;
Chifukwa iwo adzalandira,
Moyo wosatha kwa Atate.