Chichewa Christian Hymns
Hymn 438 TIYAMIKE Ambuye,
TIYAMIKE Ambuye,
Chifukwa chotilola,
Kulowa m’chaka chino m’tisunge;
Sitingathe ‘fe tokha,
Kuyenda m’chaka chonse;
Ambuye m’titsogoze,
M’tisunge.
M’tisunge, m’tisunge,
Yesu tikupemphani m’tisunge;
Ife timalephera kuyenda m’njira tokha;
Yesu tikupemphani m’tisunge.
Dziko lapansi pano timangoyenda chabe,
Wosaganiziranso za moyo;
Timaganiza kuti moyowu sudzathanso,
Ambuye m’tikumbutse leroli.
Moyowu ngwapafupi, monga kugwa kwa tsamba,
Monga kumanga mtolo m’tisunge;
Ambuye m’tidalitse,
Nthawi isanafike;
Kuti tingataike m’tisunge.