Chichewa Christian Hymns
Hymn 426 MBUYE, Mpingo wanu usauka kwakukuludi;
MBUYE, Mpingo wanu usauka kwakukuludi;
Kale lija munatsitsa Mzimu wanu Woyerawo;
Lero linonso muchite, ulimbike Mpingo wanu.
Tidza kwa Mulungu Inu, ndinu wachifundodi;
Mutipatse Mzimu wanu tsopanoli, tere lino;
Tikakhale ndi chimwemwe kuti tilimbike ndithu.
A! maliro m’Mpingo mwanu kulirira ’balewo
Adasokerera kale ndi zoipa zapadziko.
Muwabwezerenso kwanu kuti akakhalemommo.
Ndi chikondi mtithandize kuigwira nkhondoyi;
Mwa kulema ndi kulimba mutipempherere ife,
Kuti tilimbane naye Satanayo,osamwopa.
Pakubweradi Woyesa tidzamlaka ifetu;
Angelonso adzabwera kutithandizira ife,
Kuti tilimbike ife ndi kumchotsa m’mtima mwathu.
Pa la Mulungu tibwera kulandira zidazo;
Mphamvu yanu ndi chikondi zititsogolere ife;
Machitidwe ndi mkhalidwe zikokere ena kwanu.