Chichewa Christian Hymns
Hymn 397 MBUYE wathu, mutipatsa
MBUYE wathu, mutipatsa
Zonse tili nazozo,
Mutikomeratu mtima
Osaleka konseko,
Mutikonda, mutisunga,
Mutisamalira ’fe.
Dzuŵa, madzi, kudya, mpweya,
Moyo, zonse nzanuzi,
Si za ife, nzaulere,
Tingozilandiradi;
Zifumira kwa Aate
Wotikondakondatu.
Monga tilandira, Mbuye,
Mtiphunzitse tonsefe
Tipere chuma chathu
Ndi kusangalalatu;
Zakukhala m’manja mwathu
Tiziyese nzanudi.
Tikhaletu nawo, Mbuye,
Mtima wosauma ’yi
Ndi wofatsa ndi wabwino
Ndi woyerayeradi,
Kuti tiyenere Dzina
La Mbuyathu Yesuyo.
Tisaiwalire ’bale
Athu osadziŵa ’Nu,
Akulira ndi odwala
Tiŵapemphereratu;
Titsanzenso Mbuye Yesu
Ndi k’ŵathangatira ’wo.
Dalitseni, Mbuye, zonse
Zomwe taperekazi,
Mzilandire, nsembe yathu,
Mziyeretse Inudi
Ndi mitima yathu yonse
Tikuyamikirani.