Chichewa Christian Hymns
Hymn 351 CHIYEMBEKEZO changacho,
CHIYEMBEKEZO changacho,
Chamangidwa pa mwaziwo;
Sindikhulupi’ra pena,
Ndingotsamira pa Yesu.
Ndayima nji pa Khrisituyo,
Ndiye chithanthwe cholimba,
Maziko ena mpamchenga.
Ndayima nji pa Khrisituyo,
Ndiye chithanthwe cholimba,
Maziko ena mpamchenga.
Nkhope yake ‘kabisika,
Ndipuma m’chisomo chake;
M’namondwe ndi m’mphepo zonse,
Nangula wanga ali nji!
Pangano lake m’mwaziwo,
Lindisunga m’chigumula;
Zondizinga zikachoka,
Yesu ndiye Thanthwe langa.
Likalira lipengalo,
Ndipezeke mwa Yesuyo;
Wovekedwa, wolungama,
Wopanda banga konseko.