Chichewa Christian Hymns
Hymn 283 AMBUYE m’chipululu,
AMBUYE m’chipululu,
Analefuka ndi njala;
Polowa m’mayesero,
Anagonjetsatu Satana.
M’dziko lapansi lero lino,
Alipo omutsata,
Angoyima pa
Mulungu nji!
Ndizo mbewu zosawonongeka.
Nyamulani maso anu,
Muyang’ane m’kati mwanu;
Alipo anthu ena,
Oyitanidwa, nasankhidwa.
Mutawayang’ana iwo,
Akunga a umphawi;
Angoyima pa
Mulungu nji!
Ndizo mbewu zosawonongeka.
Kuwachotsa kwa Mbuye,
Satanayo walephera;
Powazunza iwotu,
Achiyesa chimwemwe ndithu.
Ambuye nawalimbikitsa,
Napukuta misozi;
Nawalonjeza koronayo,
Ndizo mbewu zosawonongeka.
Akhrisitu tilimbike,
Kugwira ntchito ya Mbuye;
Timvere mawu ake,
Tidzagonjetsatu Satana.
Pomalizatu moyo uno,
Tidzapita Kumwamba;
Tidzayimbira Mulunguyo,
Ndife mbewu zosawonongeka.