Chichewa Christian Hymns
Hymn 244 TIMVE za anamwali khumi,
TIMVE za anamwali khumi,
Okonzeka mosiyana;
Asanu anali opusa zedi,
Ena anachenjeradi.
Asanu anatenga mafuta padera,
Iwowa anachenjera,
Asanu sanatenge mafuta adera,
Iwowa anapusadi.
Mkwati pamene anafika,
Pakati pa usikuwo,
Asanu osatenga mafutawo,
Sanathe kulowa m’nyumba.
Tisakhale ngati opusa,
Osatenga mafutawo.
Tikhale ngatitu ochenjerawo,
Titenge mafuta athu.
Mbale ukhale wochenjera,
Pakulapa zoipazo;
Pakukhulupiliratu Mulungu,
Kuti tikalowe M’mwamba.