Chichewa Christian Hymns
Hymn 192 ZAKEYU mkulu wa misonkho,
ZAKEYU mkulu wa misonkho,
Nafuna kuwona Ambuye Yesu;
Nakwera mtengowo wamkuyu,
Popeza analí munthu wamfupi,
Zakeyu tsika, lero lino
Ndikadya nawe m’nyumba yako;
Chipulumutso chafika
M’nyumba ino, Ya mwana wa Brahamu.
Zakeyu napeza chisomo,
Pakukumana ndi Ambuye Yesu;
Nakhululukidwa tchimolo,
Nakhala mfulumwana wa ‘Brahamu.