Chichewa Christian Hymns
Hymn 188 MPULUMUTSI Wokondedwa,
MPULUMUTSI Wokondedwa,
Mwandipulumutsa ine;
Ndine wanu, wanu nokha,
Wotsukidwa m’mwaziwo.
Aleluya, Aleluya,
Mwanawankhosa ndinutu:
Mwazi wanu wanditsuka,
Aleluya kwa Yesu.
Mtima wanga wabvutika,
Zaka zonse ndingochimwa;
Tsono sindikangalika,
Ndingopuma mwa Yesu.
Mwandipatulira ine,
Kwa Inu ndidzipereka,
M’moyo, m’imfa mboni yanu
Ya chipulumutsocho.
Aleluya, mwandigula,
Ndipo mudzandisungabe;
Mwazi wanu ndi wamphamvu
Kuyeretsa konseko.