Chichewa Christian Hymns
Hymn 166 NDICHITENJI kukapeza
NDICHITENJI kukapeza
Moyo? thandizeni!
Ndili wakutopa; Mzimu,
Muthandize ine.
Zonse zinathedwadi;
Yesu watha zonsezo;
Sutha ntchito, ungomvera
Mawu ake omwewo.
Iye anatsika m’Mwamba,
Anachoka kwawo,
Anafera anthu, nati:
“Ndatha zonse zawo.”
Mbuye wanga ndili kumva,
Ndikondana nanu;
Umapuma mzimu wanga,
Kwathu ndiko kwanu.