Chichewa Christian Hymns
Hymn 155 UTHENGA wa Mulungu
UTHENGA wa Mulungu
Waloŵa m’mtimamu,
Wochotsa zoipazo
Zakundidetsazo.
Pakuti anthu akumvera
Yesu aŵapulumutsa,
Ine, aŵapulumutsa, indetu.
Ndidziŵa kuti Yesu
Anafa kalelo,
Nafafaniza zonse
Tinazichimwazo.
Satana ndi unyolo
Anandimanga nji!
Ambuye Yesu yekha
Nandimasuladi.
Ambuye muloŵetse
Mtendere m’mtimamo,
Ndimvetse mawu anu
Masiku onsewo.
Akuti anthu akumvera
Yesu aŵapulumutsa,
Inde, aŵapulumutsa, indetu.