Chichewa Christian Hymns
Hymn 126 DAVIDE kubusa kuja,
DAVIDE kubusa kuja,
Anaweta nkhosa zake;
Chinadza chimbalangondo,
Chowononga nkhosa.
Davide analimbika,
Nagwira chirombo chija;
Nachikhadzula kolimba,
Ndipo chinafatu.
Davide analimbika,
Sanathawe chirombocho;
Napulumutsa nkhosazo,
Zikhala ndi moyo.
Ife ndife nkhosa zake,
Za Mbuye wathu Yesuyo;
Satana monga mkangowo,
Afuna ifetu.
Yesu Mbuye adzabwera,
Muulemelero wake;
Nkhosa zake adzatenga,
Zikakhale kwawo.