Chichewa Christian Hymns
Hymn 125 ODALA ali iwo,
ODALA ali iwo,
Osauka mumzimu;
Chifukwa uli wawo,
Ufumu wa Kumwamba.
Lowa, lowani pa chipata,
Chopapatizacho,
Chakuwala mbee!
Thamanganitu m’kalandire;
Korona wa moyo,
Asanatseke.
Odala ali iwo,
Akuchita chifundo;
Chifukwa alandira,
Chifundo chachikulu.
Odala ali iwo,
Oyera mtima mwawo;
Patsiku lomaliza,
Adzawona Mulungu.
Odala ali iwo,
Akuchita mtendere;
Chifukwa adzatchedwa,
Anatu a Mulungu.
Sekera, sangalala,
Lulutira mwa Mbuye;
Chifukwa mphotho yako,
Ndi yayikulu M’mwamba.