Chichewa Christian Hymns
Hymn 489 YESU ndiye Bwenzi lathu,
YESU ndiye Bwenzi lathu,
Kumwamba kuli kwao;
Amatikonda tonse,
Akulu ndi tiana;
Anzathu sapirira
Amalekana nafe,
Komabe kutiyanja
Saleka Yesuyo.
Ana ake adzapuma
Kumwamba mokondwera,
Amene anamkonda
Namtsata Yesu yekha;
Sauko ndi zobvuta
Zotitopetsa kuno,
Sitiziona konse
Kumwamba kwathuko.
Tidzalandirabe komwe
Zobvala za mitima
Yoyera, ndi kubvula
Zakale za kuchimwa;
Chimwemwe ndi chikondi
Tidzangokhala nazo,
Za ndewu ndi chisoni Sitizipeza ’yi.
Woyenera ndani kunka
Kukhala ndi Atate,
Kuimba nyimbo zake,
Za Mpulumutsi wathu?
Tidzamka ife tonse
Tamtsata pansi pano;
Tiyeni ana onse,
Yambani leroli.