Chichewa Christian Hymns
Hymn 441 MBUYE, tikuthokozani,
MBUYE, tikuthokozani,
Ndinu mwatitsogolera;
Zaka zonse mwatisunga;
Tiyamika mokondwera,
Zotibveka, zotidyetsa,
Mphamvu, moyo, zonsezi;
’Tate tikuthokozani
Chaka chatsopanochi.
Ndinu mwatithangatira
Pakuona zosautsa;
Polefuka ndi podwala
Ndinu mwatitsitsimutsa.
Munatiteteza bwino
Tili ana kalelo,
Ndipo zomwe mwazichita
Chaka chotitheracho.
Chaka chino mutipatse
Mphamvu zosachimwa konse,
Zoipitsa ndi zodetsa
Mtima mtichotsere zonse.
Mtithandize tizimvera
Kuyambira leroli,
Ndi kugwira ntchito zanu.
Chaka chatsopanochi.
Inde,’Tate, mtiyendetse
M’njira yolungama yanu,
M’mtima mwathu mtiyeretse
Kuti tikondane nanu.
Zaka zonse muli nafe,
Sitiopa konse ’yi
’Tate tikuthokozani
Chaka chatsopanochi.