Chichewa Christian Hymns
Hymn 484 YESU ndiye Mbusa,
YESU ndiye Mbusa,
Mbusa wakukoma,
Anyamula ana
Ake akuopa;
Tizitsata Yesu,
Atitsogolera,
Kwina kuli mdima,
Kwinanso koyera.
Yesu ndiye Mbusa
Atipenyetsetsa,
Mawu ake onse
Atikondweretsa.
Mwina alangiza
Mwana wakulakwa; Atsogola bwino,
Ife tizimtsata.
Yesu ndiye Mbusa,
Anafera kale
Kuyeretsa ana
Nawo mwazi wake,
Tsono awalemba
Ndi chizindikiro;
“Ana anga onse
Andikhulupira.”
Yesu ndiye Mbusa
Wakutisunga ife,
Ali wachifundo
Chachikulu ndithu; Sitiopa imfa
Akakhala nafe,
Yesu Mbuye wathu
Alandira ife.