Chichewa Christian Hymns
Hymn 480 TIANA ife tingofoka,
TIANA ife tingofoka,
Sitikhala ’mphamvu ’yi;
Tikhoza kukachitiranji
Yesu kumkondwetsadi?
Tiana ta Ambuye tili
N’ntchito yaikuludi,
Kudzichepetsa ndi kusiya
Tchimo lili lonseli.
Kapena m’mtima ndimakwiya,
Nditukwana mnzangayo,
Kapena ndidzitama – izi
Ndilekere Mbuyeyo.
Ndileke kulimbana ndi
Kuŵanamiza enawo;
Ndinene zakufatsa,
Zakukondweretsa Yesuyo.
Tizikondana, tisekere
Tsiku lonse kwathuko,
Muyere m’mtima popeza
Yesu ndi Woyerayo.
Palibe mwana wakuchepa
Kunyamula mtandawu;
Ambuye Yesu mutipatse
Mtima wokondanatu.