Chichewa Christian Hymns
Hymn 455 TIIMBE ndi kulalikira
TIIMBE ndi kulalikira
Mthenga wa chikondicho
Anamva Mlungu m’Mwambamo
Kulira kwathu pansipa.
(Ndikhulupirira Yesu
Wobadwira m’kholamo;
Iye ndiye Mfumu yathu,
Timtame nthaŵi zonse.)
Kwa ife lero anabadwa
Mwana wa Mariyayo,
Pamsinkhu, ine mng’ono koma
Mwini dziko lonseli.
Anadza nazo mphatso zake
Anatikonzeratu; Anatitseguliradi
Pakhome pa Ufumuwo.
Ambuye takutamandani
Tsiku lakubadwali,
Mwa Inu tonse tikondwera,
Tiseke tonsefe.
A! Yesu Mbuye wakuyera,
Munagona m’kholamo;
Mudzikonzere leronso
Mogona m’mtima mwangamu.
Ulemerero m’Mwambamwamba
Ndi mtendere pansipa;
Tiimbe nafe nyimboyi,
Timyamikire Mbuyathu
(Yesu ndiye Mfumu,
Yesu ndiye Mfumu!
Ndikhulupirira Yesu wobadwira m’kholamo.)