Chichewa Christian Hymns
Hymn 448 CHIFUKWA cha zokoma mtima zonse zaulelezo,
CHIFUKWA cha zokoma mtima zonse zaulelezo,
Tim’lambire Mbuye;
Tikweze nyimbo yakukondwa kuli ‘Ye,
Tim’gwadiretu.
Dzinja lokondweretsa lafikanso, litapumatu,
Tim’lambire Mbuye;
Mvula igundanso,
Mulungu wotikonda ‘fe,
Tim’gwadiretu.
Dziko lonse lili kukondwa, mlengalenga, mpheponso,
Tim’lambire Mbuye;
Zapansi pano zonse zim’tamandire,
Mulungu wathuyo,
Tim’gwadiretu.
Maluwa abwino aphuka m’mapiri, ndi m’madambomo,
Tim’lambire Mbuye;
Masamba ‘awisi, aang’ono agwedezekanso,
Tim’gwadiretu.
Zanu zapansi n’zokoma
Mbuye; tikondwera ‘fe,
Tim’lambire Mbuye;
Koma kwanu Kumwamba komwe kwapambanatu,
Tim’gwadiretu.
Nafenso tidzauka kwa
‘kufa ngati maluwawo,
Tim’lambire Mbuye;
Oyera mtima adzavala mbuu! pakudza Khrisituyo,
Tim’gwadiretu.
Tidzakhala naye nthawi zonse, ndi kuyimbako,
Tim’lambire Mbuye;
Kumene moyo wa anthu okhululukidwa uli wokomatu,
Tim’gwadiretu.
Aleluya, Amen!