Chichewa Christian Hymns
Hymn 432 KRISTU ndiye Mwala wathu,
KRISTU ndiye Mwala wathu,
Kristu timangirapo;
Wosankhidwa ndi Mulungu,
Atimange tonsefe;
Iye ndi Mthandizi wathu,
Timkhulupirira ’Ye
Mudalitse nyumba yathu;
Mbuye, nthaŵi zonsetu
Muthandize anthu onse
Odza kuphunzira ’mu,
Ndi antchito anu omwe
Odza k’ŵaphunzitsa ’mu.
Tiyamike Mlungu ’Tate,
Tiyamike Mwanayo,
Tiyamike Mzimu wake;
Onse omwe Mmodzitu,
Waulemerero wonse
Ndi wamphamvu ponsepo.