Chichewa Christian Hymns
Hymn 382 M’wabatize anzathuwa,
M’wabatize anzathuwa,
Ndi Mzimu wanu Woyera;
Chikhale chizindikiro,
Cha chikondi chanu chija.
Batizeni, batizeni!
Batizeni, batizeni!
Ndi Mzimu wanu Woyera!
Pobatizidwa ndi madzi,
M’wabatizenso ndi mwazi;
Kuwayeretsa mitima,
Ndi mwazi wanu womwewo.
Tifike tonse kumtsinje,
Wamwazi wa Mbuye Yesu;
Tiyeretsedwe tonsefe,
Ndi mwazi wanu womwewo.
Tibatizeni tonsefe,
Ndi Mzimu wanu Woyera;
Chikhale chizindikiro,
Cha chikondi chanu chija.