Chichewa Christian Hymns
Hymn 350 MBUYE ndayima pano,
MBUYE ndayima pano,
Ndamva zakudza kwanu;
Ine ndidikilira, sinditopa,
Mpaka Inu mutabwera.
(M) Kaya imfa
(O) Ine ndidikilira,
(M) Kaya nkhondo
(O) Ine ndidikilira;
(M) Kaya njala
(O) Ine ndidikilira, sinditopa mpaka inu mutabwera.
Mbuye dziko lapansi,
Munagonjetsa kale;
Zonse zilibe mphamvu,
Sinditopa mpaka Inu mutabwera.
Ine ndidikilira,
Chondiwopsa palibe;
Poti ndili mwa Inu,
Sinditopa mpaka Inu mutabwera.